Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.
Numeri 8:10 - Buku Lopatulika nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israele aike manja ao pa Alevi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israele aike manja ao pa Alevi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ukuŵapereka Aleviwo pamaso pa Chauta, Aisraele asanjike manja ao pa Alevi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ubwere nawo pamaso pa Yehova, ndipo Aisraeli asanjike manja awo pa iwo. |
Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.
Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.
Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova.
Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.
Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.