Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 4:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Apo atsogoleri a mpingo asanjike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Chauta, ndipo aiphe pamaso pa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Akuluakulu a anthuwo asanjike manja awo pa mutu pa ngʼombe pamaso pa Yehova, ndipo ayiphe pomwepo pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 4:15
16 Mawu Ofanana  

Pamenepo anayandikiza nao atonde a nsembe yauchimo pamaso pa mfumu ndi msonkhano; ndipo iwo anawasanjika manja ao,


Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;


Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri anakwerako;


Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.


Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.


ndipo Aroni aike manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israele, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,


Ndipo wansembe wodzozedwayo adze nao mwazi wina wa ng'ombeyo ku chihema chokomanako;


Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la chihema chokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.


Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo.


Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.


Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa mphongoyo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.


Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena naye, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akulu makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.


nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israele aike manja ao pa Alevi;


Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa