Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 6:6 - Buku Lopatulika

6 amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Adaŵaimiritsa pamaso pa atumwi, ndipo atumwiwo adapemphera naŵasanjika manja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iwo anapereka anthuwa kwa atumwi amene anawapempherera ndi kuwasanjika manja.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 6:6
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;


nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israele aike manja ao pa Alevi;


nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo.


Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,


Pamenepo, m'mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.


Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.


Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.


ndipo anaona mwamuna dzina lake Ananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.


Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose.


Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.


Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga.


a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa