Numeri 8:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anawuza Mose kuti, |
Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye.
Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikaponyalicho.
Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.