Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.
Numeri 7:8 - Buku Lopatulika napatsa ana a Merari magaleta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa ntchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 napatsa ana a Merari magaleta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa ntchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Merari adaŵapatsa ngolo zinai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu potsata ntchito yao, imene woyang'anira wake anali Itamara, mwana wa wansembe Aroni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndiponso anapereka ngolo zinayi ndi ngʼombe zothena zisanu ndi zitatu kwa Amerari molingananso ndi ntchito yawo. Onsewa ankawayangʼanira anali Itamara mwana wa Aaroni wansembe. |
Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.