Sindikudzudzula iwe chifukwa cha nsembe zako; popeza nsembe zako zopsereza zili pamaso panga chikhalire.
Numeri 7:45 - Buku Lopatulika ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, chopereka cha nsembe yopsereza: |
Sindikudzudzula iwe chifukwa cha nsembe zako; popeza nsembe zako zopsereza zili pamaso panga chikhalire.
Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.
Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde.
Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa.
Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.