Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 66:15 - Buku Lopatulika

15 Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ndidzapereka kwa Inu nsembe zopsereza za nyama zonenepa, utsi wa nsembe za nkhosa zamphongo udzafika kwa Inu. Ndidzaperekanso ngati nsembe ng'ombe zamphongo ndi mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu ndi chopereka cha nkhosa zazimuna; ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 66:15
8 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pamene akunyamula likasa la Yehova atayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye anapha nsembe ng'ombe ndi chonenepa china.


Otengedwa ndende, atatuluka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisraele onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, anaankhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.


Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu; pamenepo adzapereka ng'ombe paguwa lanu la nsembe.


anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.


pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika;


ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa