Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona.
Numeri 7:31 - Buku Lopatulika chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika, zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika, zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ndi zopereka za zakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka chachakudya. |
Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona.
Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.