Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 25:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Upange mbale ndi zipande zofunika popereka lubani, ndiponso mitsuko ndi mabeseni ofunika pa zopereka za chakumwa. Zonsezi zikhale za golide wabwino kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Upange mbale ndi zipande zagolide wabwino, pamodzinso ndi mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 25:29
14 Mawu Ofanana  

ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira moto za golide woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolide, za zitseko za chipinda cha m'katimo, malo opatulika kwambiri, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kachisi.


ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golide woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zake za m'katimo za malo opatulika kwambiri, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kachisi, zinali zagolide.


Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome.


Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo, za golide woona.


Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.


Ndi pa gome la mkate woonekera ayale nsalu yamadzi, naikepo mbale zake, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa chikhalire uzikhalaponso.


chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;


anabwera nacho chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;


Uku ndi kupereka chiperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israele, tsiku la kudzoza kwake: mbale zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolide khumi ndi ziwiri;


Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa