Asadzidetse ndi atate wake, kapena mai wake, mbale wake, kapena mlongo wake, akafa iwowa; popeza chowindira Mulungu wake chili pamutu pake.
Numeri 6:8 - Buku Lopatulika Masiku onse a kusala kwake akhala wopatulikira kwa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku onse a kusala kwake akhala wopatulikira kwa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthuyo ndi wopatulikira Chauta masiku onse a kudzipereka kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthuyo ndi wopatulika masiku onse odzipereka kwake kwa Yehova. |
Asadzidetse ndi atate wake, kapena mai wake, mbale wake, kapena mlongo wake, akafa iwowa; popeza chowindira Mulungu wake chili pamutu pake.
Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete.
Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye;
chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.