Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 6:9 - Buku Lopatulika

9 Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ngati munthu wina aliyense afa mwadzidzidzi pafupi naye, ndipo pakutero aipitsa tsitsi lake loperekedwalo, amete kumutu kwake pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku lomuyeretsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Ngati munthu wina afa mwadzidzidzi pafupi naye ndi kudetsa tsitsi lake loperekedwalo, amete mutu wake pa tsiku lodziyeretsa, tsiku lachisanu ndi chiwiri.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:9
11 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yake yauchimo, ati Ambuye Yehova.


Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lake lonse la pamutu pake, ndi ndevu zake, ndi nsidze zake, inde amete tsitsi lake lonse; natsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nakhale woyera.


Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wake wa kusala kwake pa khomo la chihema chokomanako, natenge tsitsi la pamutu wake wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.


Masiku onse a kusala kwake akhala wopatulikira kwa Yehova.


Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.


Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye mu Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,


pamenepo mufike naye kwanu kunyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pake, ndi kuwenga makadabo ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa