Ndipo asayandikire kwa munthu aliyense wakufa, angadzidetse; koma chifukwa cha atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.
Numeri 6:7 - Buku Lopatulika Asadzidetse ndi atate wake, kapena mai wake, mbale wake, kapena mlongo wake, akafa iwowa; popeza chowindira Mulungu wake chili pamutu pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Asadzidetse ndi atate wake, kapena mai wake, mbale wake, kapena mlongo wake, akafa iwowa; popeza chowindira Mulungu wake chili pamutu pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asadziipitse poyandikira mtembo wa bambo wake, wa mai wake, wa mbale wake kapena wa mlongo wake, chifukwa kulumbira kwa kudzipereka kwake kwa Mulungu kuli pamutu pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake. |
Ndipo asayandikire kwa munthu aliyense wakufa, angadzidetse; koma chifukwa cha atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.
Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;