Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.
Numeri 5:4 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Israele anachita chotero, nawatulutsira kunja kwa chigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israele anachita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Israele anachita chotero, nawatulutsira kunja kwa chigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israele anachita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Aisraele adachitadi zimenezi, ndipo adaŵatulutsira kunja anthuwo. Ankachitadi monga momwe Chauta adaauzira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli anachitadi zimenezi. Anawatulutsira kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose. |
Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.
Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.
Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.
muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo.