Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wamwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika,
Numeri 5:19 - Buku Lopatulika Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukire kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono amlumbiritse mkaziyo kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sadagone nawe, ndipo ngati sudachite kanthu kokuipitsa pamene unali m'manja mwa mwamuna wako, madzi oŵaŵa ali apaŵa usatenge nawo matemberero. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka wansembeyo alumbiritse mkaziyo ndi kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sanagonane ndi iwe ndipo sunayende njira yoyipa ndi kukhala wodetsedwa pomwe uli pa ukwati ndi mwamuna wako, madzi owawa awa omwe amabweretsa temberero asakupweteke. |
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wamwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika,
Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.
Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.
Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.