Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao.
Numeri 5:17 - Buku Lopatulika natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko fumbi lili pansi mu chihema, wansembeyo nalithire m'madzimo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko fumbi lili pansi m'Kachisi, wansembeyo nalithire m'madzimo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wansembeyo atengeko madzi oyera m'mbiya, ndipo atapeko fumbi la m'Chihema cha Mulungu ndi kulithira m'madzimo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo wansembeyo atenge madzi oyera mʼmbiya ya dothi ndi kuyika mʼmadzimo fumbi lapansi la mʼTenti ya Msonkhano. |
Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao.
Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa chihema chokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.
Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.
Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.