Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.
Numeri 5:16 - Buku Lopatulika Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Wansembe abwere ndi mkaziyo pafupi ndi kumuimika pamaso pa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Wansembe abwere naye mkaziyo ndi kumuyimitsa pamaso pa Yehova. |
Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.
Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.
pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.
natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko fumbi lili pansi mu chihema, wansembeyo nalithire m'madzimo.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.