ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.
Numeri 5:10 - Buku Lopatulika Zopatulika za munthu aliyense ndi zake: zilizonse munthu aliyense akapatsa wansembe, zisanduka zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zopatulika za munthu aliyense ndi zake: zilizonse munthu aliyense akapatsa wansembe, zasanduka zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zopereka zopatulika za munthu aliyense, nzake za iye yemweyo. Koma chilichonse chimene munthu apereka kwa wansembe, nchake cha wansembeyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mphatso zilizonse zopatulika ndi za munthuyo, koma zomwe wapereka kwa wansembe ndi za wansembeyo.’ ” |
ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.
ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza chotero.
Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.