Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 4:9 - Buku Lopatulika

Ndipo atenge nsalu yamadzi, ndi kuphimba choikaponyali younikira, ndi nyali zake, ndi mbano zake, ndi zoolera zake, ndi zotengera zake zonse za mafuta zogwira nazo ntchito yake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo atenge nsalu yamadzi, ndi kuphimba choikapo nyali younikira, ndi nyali zake, ndi mbano zake, ndi zoolera zake, ndi zotengera zake zonse za mafuta zogwira nazo ntchito yake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atenge nsalu yobiriŵira ndi kuphimba choikaponyale, pamodzi ndi nyale zake, mbaniro zake, mbale za phulusa ndi ziŵiya zake zonse za mafuta.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Azitenga nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira choyikapo nyale, pamodzi ndi nyale zake, zopanira zake, zotengera zake ndi mitsuko yonse yosungiramo mafuta.

Onani mutuwo



Numeri 4:9
8 Mawu Ofanana  

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.


Ndipo achimange ndi chipangizo zake zonse m'chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa chonyamulira.


Ndipo ayale pa izi nsalu yofiira, ndi kuliphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.


Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.