Numeri 4:41 - Buku Lopatulika Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Geresoni, onse akutumikira m'chihema chokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Geresoni, onse akutumikira m'chihema chokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chimenechi ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'banja a Ageresoni, amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ichi chinali chiwerengero cha Ageresoni mwa mabanja awo amene ankatumikira ku tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova. |
owerengedwa ao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.
Ndipo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,
Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.