Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
Numeri 4:34 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Aroni ndi akalonga a khamu anawerenga ana a Akohati monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Aroni ndi akalonga a khamu anawerenga ana a Akohati monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a mpingo, adaŵerenga ana a Akohati potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose, Aaroni ndi atsogoleri a magulu a anthu anawerenga Akohati monga mwa mafuko ndi mabanja awo. |
Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mafuko onse; yense mkulu wa nyumba ya kholo lake.
Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.
Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe.
kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito m'chihema chokomanako;