Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 4:11 - Buku Lopatulika

Ndipo paguwa la nsembe lagolide aziyala nsalu ya madzi, naliphimbe ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo pa guwa la nsembe lagolide aziyala nsalu ya madzi, naliphimbe ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ayale nsalu yobiriŵira pa guwa lagolide, ndi kuliphimba ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira.

Onani mutuwo



Numeri 4:11
9 Mawu Ofanana  

ndi guwa la nsembe lagolide, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho;


Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lagolide chakuno cha likasa la mboni, numange pa chihema nsalu yotsekera pakhomo.


Ndipo achimange ndi chipangizo zake zonse m'chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa chonyamulira.


Natenge zipangizo zake zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsalu yamadzi, ndi kuziphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pachonyamulira.


ndi kuikapo chophimba cha zikopa za akatumbu; ndi kuyalapo nsalu yamadzi yeniyeni, ndi kupisako mphiko zake.


Ndipo anadza mngelo wina, naima paguwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse paguwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.