Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 4:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Ndipo paguwa la nsembe lagolide aziyala nsalu ya madzi, naliphimbe ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo pa guwa la nsembe lagolide aziyala nsalu ya madzi, naliphimbe ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ayale nsalu yobiriŵira pa guwa lagolide, ndi kuliphimba ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:11
9 Mawu Ofanana  

guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani onunkhira ndi nsalu yotchinga pa khomo lolowera mu tenti;


Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema.


Kenaka achikulunge pamodzi ndi zipangizo zake zonse mʼzikopa za akatumbu ndi kuchiyika pa chonyamulira chake.


“Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake.


Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.


Mngelo wina amene anali ndi chofukizira chagolide anabwera nayimirira pa guwa lansembe. Anapatsidwa lubani wambiri kuti amupereke pamodzi ndi mapemphero a anthu onse oyera mtima pa guwa lansembe lagolide patsogolo pa mpando waufumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa