Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.
Numeri 36:7 - Buku Lopatulika Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko; popeza ana a Israele adzamamatira yense ku cholowa cha fuko la makolo ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko; popeza ana a Israele adzamamatira yense ku cholowa cha fuko la makolo ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choloŵa cha Aisraele chisachotsedwe m'fuko lina nkuchipatsa fuko lina. Pakuti Mwisraele aliyense ayenera kukangamira pa choloŵa cha fuko la makolo ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti cholowa cha Israeli chisapite ku fuko lina, pakuti Mwisraeli aliyense ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake. |
Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.
Ndipo mwana wamkazi yense wa mafuko a ana a Israele, wakukhala nacho cholowa, akwatibwe ndi wina wa banja la fuko la kholo lake, kuti ana a Israele akhale nacho yense cholowa cha makolo ake.
Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake.
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.