Numeri 36:9 - Buku Lopatulika9 Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Choncho palibe choloŵa chimene chidzachotsedwe m'fuko lina kupatsidwa ku fuko lina. Pajatu fuko lililonse la Aisraele lidzakangamira pa choloŵa chake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Cholowa chilichonse mu Israeli sichiyenera kupita ku fuko lina, popeza fuko lililonse la Israeli liyenera kusunga cholowa chimene linalandira.” Onani mutuwo |
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.