Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 34:6 - Buku Lopatulika

Kunena za malire a kumadzulo Nyanja Yaikulu ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Kunena za malire a kumadzulo Nyanja Yaikulu ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Malire anu akuzambwe akhale Nyanja Yaikulu ndi gombe lake. Ameneŵa ndiwo malire akuzambwe.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.

Onani mutuwo



Numeri 34:6
12 Mawu Ofanana  

Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.


Ndipo malire a dzikoli ndi awa: mbali ya kumpoto, kuyambira ku Nyanja Yaikulu, kutsata njira ya ku Hetiloni, kufikira polowera ku Zedadi;


Ndi mbali ya kumadzulo ndiyo Nyanja Yaikulu, kuyambira malire a kumwera kufikira pandunji polowera ku Hamati. Ndiyo mbali ya kumadzulo.


ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kunka ku mtsinje wa Ejipito, ndi kutuluka kwao adzatuluka kunyanja.


Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku Nyanja Yaikulu mulinge kuphiri la Hori:


ndi Nafutali lonse, ndi dziko la Efuremu, ndi Manase, ndi dziko lonse la Yuda, kufikira nyanja ya m'tsogolo;


Kuyambira chipululu, ndi Lebanoni uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Yufurate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.


natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja.


Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikulu ndiwo malire ake. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.


Asidodi, mizinda yake ndi midzi yake; Gaza, mizinda yake ndi midzi yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.


Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale cholowa cha mafuko anu, kuyambira ku Yordani, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa.


Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;