Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m'chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe.