ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yowele, wokhala ku Aroere, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-Meoni;
Numeri 32:34 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroere; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroere; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Gadi adamanga mizinda ya Diboni, Ataroti, Aroere, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Agadi anamanga Diboni, Ataroti, Aroeri, |
ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yowele, wokhala ku Aroere, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-Meoni;
atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.
Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa. Ndiwo wakufikira ku Medeba.
Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,
Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mzinda wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.
nawakantha kuyambira ku Aroere mpaka ufika ku Miniti, ndiyo mizinda makumi awiri, ndi ku Abele-Keranimu, makanthidwe aakulu ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israele.