Numeri 32:33 - Buku Lopatulika33 Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi hafu la fuko la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi mizinda yake m'malire mwao, ndiyo mizinda ya dziko lozungulirako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201433 Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi fuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi midzi yake m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa33 Pomwepo Mose adapatsa ana a Gadi ndi a Rubeni ndiponso theka la fuko la Manase, mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dziko lonse pamodzi ndi mizinda ndi milaga yake, ndiye kuti mizinda yonse ya m'dziko lonselo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero33 Choncho Mose anapatsa Agadi, Arubeni ndi theka la fuko la Manase mwana wa Yosefe dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi, mfumu ya ku Basani, dziko lonse, mizinda yake ndi midzi yowazungulira. Onani mutuwo |