Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 32:32 - Buku Lopatulika

32 Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma cholowa chathuchathu chikhale tsidya lino la Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma cholowa chathuchathu chikhale tsidya lino la Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Tidzaoloka titatenga zida zankhondo pamaso pa Chauta, ndi kuloŵa m'dziko la Kanani, koma chuma cha choloŵa chathu chidzatsala ndi ife konkuno ku tsidya lino la Yordani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Tidzawoloka pamaso pa Yehova ndipo tidzalowa mu Kanaani ndi zida zankhondo, koma cholowa chathu chidzakhala ku tsidya lino la Yorodani.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 32:32
10 Mawu Ofanana  

Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu;


Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m'tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum'mawa.


Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzachita.


Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi hafu la fuko la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi mizinda yake m'malire mwao, ndiyo mizinda ya dziko lozungulirako.


mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa.


Awa ndi mau amene Mose ananena kwa Israele wonse, tsidya la Yordani m'chipululu, m'chidikha cha pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofele, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Dizahabu.


ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale cholowa chao cha Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase.


Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroere, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Giliyadi, ndi mizinda yake, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi.


Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israele anawakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordani kum'mawa, kuyambira chigwa cha Arinoni, mpaka phiri la Heremoni, ndi chidikha chonse cha kum'mawa;


Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi hafu la fuko la Manase, likhale cholowa chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa