Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.
Numeri 30:5 - Buku Lopatulika Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma bambo wake akamkaniza mwanayo pa tsiku lomwe wamva zimenezo, palibe lamulo lomkakamiza mwanayo kuti achite zimene adalumbirazo ndi zimene adalonjezazo. Chauta adzamkhululukira mwanayo chifukwa choti bambo wake adamkaniza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati abambo akewo amva kulumbira kwake ndi kumukaniza, palibe lamulo lomukakamiza mkaziyo kuchita zimene walonjeza. Yehova adzamukhululukira chifukwa abambo ake anamukaniza. |
Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.
ndipo mwamuna wake anamva, koma anakhala naye chete osamletsa, pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.
ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga nacho moyo wake, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika.
Ndipo akakwatibwa naye mwamuna, pokhala ali nazo zowinda zake, kapena zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake;
Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira.