Numeri 3:27 - Buku Lopatulika Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aamuramu, Aizari, Ahebroni ndi Auziyele, anali mabanja otuluka mwa Kohati. Ameneŵa ndiwo amene anali mabanja a Akohati. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa Kohati kunali mabanja a Amramu, Aizihara, Ahebroni ndi Auzieli. Awa ndiye anali mabanja a Akohati. |
A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake odziwa mphamvu chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang'anira Israele tsidya lino la Yordani kumadzulo, kuyang'anira ntchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu.
ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse.
Powawerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi, akusunga udikiro wa pamalo opatulika.
Werengani ana a Kohati pakati pa ana a Levi, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,
Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Efuremu, ndi pa fuko la Dani, ndi pa hafu la fuko la Manase, mizinda khumi.