Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.
Numeri 3:23 - Buku Lopatulika Mabanja a Ageresoni azimanga mahema ao pambuyo pa chihema kumadzulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mabanja a Ageresoni azimanga mahema ao pambuyo pa Kachisi kumadzulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mabanja a Geresoni ankamanga zithando zao kumbuyo kwa chihema cha Mulungu mbali yakuzambwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mabanja a Ageresoni azimanga misasa yawo kumadzulo, kumbuyo kwa Chihema. |
Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.
Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao.
Owerengedwa ao, powawerenga amuna onse, kuyambira mwana wa mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.