Numeri 28:16 - Buku Lopatulika Ndipo mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi pali Paska wa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi pali Paska wa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tsiku la 14 la mwezi woyamba, ndi la Paska ya Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova. |
Mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chinai madzulo ake, muzidya mkate wopanda chotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ake.
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.
Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye?
Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paska afika, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda.