Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 28:15 - Buku Lopatulika

15 Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yauchimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yauchimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta. Aipereke kuwonjezera pa nsembe zopsereza ndi zopereka za zakumwa za tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Powonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake cha chakumwa, mbuzi yayimuna imodzi iperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopepesera machimo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 28:15
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga malaya ake a Yosefe, napha tonde, naviika malaya m'mwazi wake:


Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m'tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo;


nachitire chotetezera malo opatulika, chifukwa cha kudetsedwa kwa ana a Israele, ndi chifukwa cha zolakwa zao, monga mwa zochimwa zao zonse; nachitire chihema chokomanako momwemo, chakukhala nao pakati pa zodetsa zao.


akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake, ndicho tonde wopanda chilema;


pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.


Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka.


ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, yakutetezera inu.


Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.


tonde mmodzi wakutetezera inu.


ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.


ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo, yakutetezera inu;


Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa