Numeri 28:14 - Buku Lopatulika14 Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Chopereka cha chakumwa chikhale cha vinyo wokwanira malita aŵiri pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ya vinyo wokwanira lita limodzi ndi theka pa nkhosa yamphongoyo, ndi ya vinyo wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse, pa miyezi yonse ya chaka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka. Onani mutuwo |