Numeri 27:4 - Buku Lopatulika Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi dzina la bambo wathu life chifukwa choti analibe mwana wamwamuna? Mutipatse choloŵa chathu pakati pa abale a bambo wathu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chiyani dzina la abambo athu lasowa pakati pa fuko lawo, kodi popeza analibe mwana wamwamuna? Tipatseni cholowa chathu pakati pa abale a abambo athu.” |
Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?
Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.
Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao.