Numeri 27:3 - Buku Lopatulika3 Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana amuna. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 “Bambo wathu adafera m'chipululu. Iyeyo sanali nao m'gulu la anthu aja amene adasonkhana pamodzi ndi Kora naukira Chauta, iye adafera tchimo lake, koma analibe ana aamuna. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 “Abambo athu anafera mʼchipululu koma sanali nawo mʼgulu la anthu otsatira Kora, omwe anasonkhana pamodzi kutsutsana ndi Yehova. Abambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo ndipo sanasiye ana aamuna. Onani mutuwo |