Numeri 27:11 - Buku Lopatulika
Ndipo akapanda abale a atate wake, mupatse wa chibale wake woyandikizana naye wa fuko lake cholowa chake, likhale lakelake; ndipo likhale kwa ana a Israele lemba monga Yehova wamuuza Mose.
Onani mutuwo
Ndipo akapanda abale a atate wake, mupatse wa chibale chake woyandikizana naye wa fuko lake cholowa chake, likhale lakelake; ndipo likhale kwa ana a Israele lemba monga Yehova wamuuza Mose.
Onani mutuwo
Bambo wakeyo akakhala wopanda abale, choloŵa chakecho upatse wachibale wake pabanja pakepo, ndipo chidzakhala chake. Ameneŵa akhale malamulo ndi malangizo kwa Aisraele, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.’ ”
Onani mutuwo
Ngati abambo ake analibe mʼbale, muzipereka cholowa chakecho kwa mnansi wake wa mʼbanja lake kuti chikhale chake. Ili likhale lamulo kwa Aisraeli, monga momwe Yehova analamulira Mose.’ ”
Onani mutuwo