Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.
Numeri 26:61 - Buku Lopatulika Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Nadabu ndi Abihu adafa chifukwa adaapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo). |
Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.
Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.