Numeri 3:4 - Buku Lopatulika4 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Koma Nadabu ndi Abihu adafa pamaso pa Chauta pamene adapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta m'chipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana, ndipo choncho Eleazara ndi Itamara adatumikira pa ntchito yaunsembe pa nthaŵi imene Aroni bambo wao anali moyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo. Onani mutuwo |