Ndi ana aamuna a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele.
Numeri 26:44 - Buku Lopatulika Ana aamuna a Asere monga mwa mabanja ao ndiwo: Imina, ndiye kholo la banja la Aimina; Isivi, ndiye kholo la banja la Aisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana amuna a Asere monga mwa mabanja ao ndiwo: Imina, ndiye kholo la banja la Imina; Isivi, ndiye kholo la banja la Aisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Potsata mabanja ao ana aamuna a Asere anali aŵa: Imina, anali kholo la banja la Aimina. Isivi anali kholo la banja la Aisivi. Beriya anali kholo la banja la Aberiya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna; kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi; kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya; |
Ndi ana aamuna a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele.
A ana a Asere, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Ana a Beriya ndiwo: Hebere, ndiye kholo la banja la Ahebere; Malikiele, ndiye kholo la banja la Amalikiele.