Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.
Numeri 26:4 - Buku Lopatulika Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Muchite chiŵerengero cha anthu, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo,” monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Aisraele amene adatuluka m'dziko la Ejipito anali aŵa: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa: |
Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.
Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti,
Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana aamuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;