Numeri 26:38 - Buku Lopatulika Ana aamuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibele, ndiye kholo la banja la Aasibele; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana amuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibele, ndiye kholo la banja la Aasibele; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Potsata mabanja ao ana aamuna a Benjamini anali aŵa: Bela anali kholo la banja la Abela. Asibele anali kholo la banja la Aasibele. Ahiramu anali kholo la banja la Aahiramu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Bela, fuko la Abela; kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli; kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu; |
Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.
Ndipo Benjamini anabala Bela mwana wake woyamba, Asibele wachiwiri, ndi Ahara wachitatu,
A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana aamuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.
ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.