Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 26:29 - Buku Lopatulika

Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Giliyadi; ndiye kholo la banja la Agiliyadi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Giliyadi; ndiye kholo la banja la Agiliyadi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ana aamuna a Manase anali aŵa: Makiri anali kholo la banja la Amakiri. Makiri anali bambo wa Giliyadi. Giliyadi anali kholo la banja la Agiliyadi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zidzukulu za Manase: kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi); kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi.

Onani mutuwo



Numeri 26:29
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pamutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pamutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.


Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.


Ndipo pambuyo pake Hezironi analowa kwa mwana wamkazi wa Makiri atate wa Giliyadi, amene anamtenga akhale mkazi wake, pokhala wa zaka makumi asanu ndi limodzi mwamunayo; ndipo mkaziyo anambalira Segubu.


Ndipo akulu a makolo a mabanja a ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akulu a makolo a ana a Israele;


Ndipo ndinampatsa Makiri Giliyadi.


Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.


Anafika Aefuremu amene adika mizu mu Amaleke; Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako. Ku Makiri kudachokera olamulira, ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.