Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 48:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pamutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pamutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pa mutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pa mutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma Yakobe adasemphanitsa manja. Motero adasanjika dzanja lake lamanja pamutu pa Efuremu amene anali wamng'ono, dzanja lamanzere adalisanjika pamutu pa Manase amene anali wamkulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma Israeli anapinganitsa mikono motero kuti anayika dzanja lake lamanja pamutu pa Efereimu ngakhale kuti iyeyo anali wamngʼono ndi dzanja lake lakumanzere analisanjika pamutu pa Manase ngakhale kuti iyeyu ndiye anali mwana woyamba.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 48:14
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.


Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.


Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.


Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efuremu m'dzanja lake lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m'dzanja lake lamanzere ku dzanja lamanja la Israele, nadza nao pafupi ndi iye.


Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pamutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pamutu wa Efuremu ndi kuliika pamutu wa Manase.


Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pamutu wake.


Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


Dzanja lamanja la Yehova likwezeka, Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu.


Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.


Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.


nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israele aike manja ao pa Alevi;


Ndipo ndatenga Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele.


Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.


Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.


Ndipo Iye anaika manja ake pa ito, nachokapo.


Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


Ndipo anaika manja ake pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.


Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundumitundu, anadza nao kwa Iye; ndipo Iye anaika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa.


Pamenepo, m'mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.


amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose.


Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.


Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa