Koma dzina la Mwisraele adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidiyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba ya makolo mwa Asimeoni.
Numeri 26:14 - Buku Lopatulika Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana ziwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana ziwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneŵa, anthu okwanira 22,200, ndiwo a m'mabanja a Simeoni, amene adaŵerengedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200. |
Koma dzina la Mwisraele adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidiyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba ya makolo mwa Asimeoni.
Ana aamuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Suni;
Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.