Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.
Numeri 23:14 - Buku Lopatulika Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapita naye ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga, namangapo maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo adapereka nsembe ya ng'ombe yamphongo ndi nsembe ya nkhosa yamphongo pa guwa lililonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono anamutengera ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo kumeneko anamanga maguwa ansembe asanu ndi awiri ndipo anapereka nsembe ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse. |
Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.
Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; mu Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda.
atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.
Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.
Ndipo anati kwa Balaki, Imani pano pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine ndikakomane ndi Iye uko.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
Kwera kumwamba ku Pisiga, nukweze maso ako kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, nuyang'ane ndi maso ako; popeza sudzaoloka Yordani uyo.
Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani;
ndi chidikha chonse tsidya lija la Yordani kum'mawa, kufikira ku Nyanja ya Araba, pa tsinde lake la Pisiga.