Hoseya 12:11 - Buku Lopatulika11 Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; mu Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; m'Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Komabe anthu ankapembedza mafano ku Giliyadi. Ndithu mafano ameneŵa adzaonongedwa. Ankapereka nsembe za nkhunzi ku Giligala, koma maguwa ansembewo ndidzaŵasandutsa miyulu ya miyala m'munda.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Kodi Giliyadi ndi woyipa? Anthu ake ndi achabechabe! Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala? Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala mʼmunda molimidwa. Onani mutuwo |
Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.