Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake kwa wakuka wanga Sarai.
Numeri 22:9 - Buku Lopatulika Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Mulungu adadza kwa Balamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iweŵa ndani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anabwera kwa Balaamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iwewa ndani?” |
Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake kwa wakuka wanga Sarai.
Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.
Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga?
Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao.
Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.
Ndipo Balamu anati kwa Mulungu, Balaki mwana wa Zipori mfumu ya Mowabu, anatumiza kwa ine, ndi kuti,
Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.
Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu.
chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?
Koma ichi sananene kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho ananenera kuti Yesu adzafera mtunduwo;