Genesis 16:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake kwa wakuka wanga Sarai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake kwa wakuka wanga Sarai. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Ndipo adati, “Iwe Hagara, mdzakazi wa Sarai, kodi ukuchokera kuti, nanga ukupita kuti?” Iye adayankha kuti “Ndikuthaŵa mbuyanga Sarai.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Ndipo mngeloyo anati, “Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?” Iye anayankha, “Ndikuthawa mbuye wanga Sarai.” Onani mutuwo |
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.